Psalms 125

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Amene amadalira Yehova ali ngati phiri la Ziyoni,
limene silingagwedezeke koma ndi lokhala mpaka muyaya.
2Monga mapiri azungulira Yerusalemu,
momwemonso Yehova azungulira anthu ake
kuyambira tsopano mpaka muyaya.

3Ndodo yaufumu ya anthu oyipa sidzakhala
pa dziko limene lapatsidwa kwa anthu olungama,
kuti anthu olungamawo
angachite nawonso zoyipa.

4Yehova chitirani zabwino amene ndi abwino,
amene ndi olungama mtima
5Koma amene amatembenukira ku njira zokhotakhota,
Yehova adzawachotsa pamodzi ndi anthu ochita zoyipa.

Mtendere ukhale pa Israeli.
Copyright information for NyaCCL